Chidziwitso : Tsiku Losesa, Kuchotsa Zinyalala ndi Kukonza malo
Khonsolo ya mzinda wa Lilongwe ikukumbutsa anthu onse mu mzindawu kuti tsiku losesa, kuchotsa zinyalala ndi kukonza malo mwezi uno likhalapo lero pa 11 February 2022 kuyambira nthawi ya 2 koloko masana mpaka 5 koloko madzulo.
Khonsoloyi ikupempha atsogoleli onse a: m’ma ofesi a boma, mabungwe oziyimira pa okha, makampani, a Mpingo, Makhansala, Mafumu ndi ena onse kuti azatsogolere ntchitoyi mumadera awo.
Khonsoloyi ikukumbutsanso anthu onse kuti azabweretse zipangizo zogwirira ntchitoyi monga masache, makasu, ndi zida zina zoyenelera; kuphatikizapo zodzitchinjilizira kunkhope zoti adzagwilitse ntchito, ndikudzitetezera panthawiyi.
Dziwani kuti makampani kapena mabungwe ali ndi ufulu wosankha komwe afuna akagwire ntchitoyi; ndipo adziwitse mwansanga a Khonsoloyi.
Khonsoloyi ikukumbutsa anthu onse kuti azatsatire njira zonse zopewera matenda a Korona (Covid-19) pogwira ntchitoyi.
Kuti mudziwe zambiri imbirani foni a Thokozani Mkaka pa nambala iyi: 0999572208/0888572208 kapena a Benson Chidaomba pa nambala iyi: 0999375166.
Kumbukirani kuti kusunga ukhondo wa mzinda wa Lilongwe ndi udindo wa aliyense.