
Kuletsa kugulitsa Dowe/ Mondokwa
Khonsolo ya Mzinda wa Lilongwe ikudziwitsa anthu onse okhala mu Mzindawu kuti kugulitsa (Dowe/ Mondokwa )mumzindawu kwaletsedwa.
Lamuloli likhala likugwira ntchito kufikira chimanga chakumunda chitakololedwa.
Aliyense opezeka akugulitsa dowe/ mondokwa mumzindawu adzalandira chilango monga mwa malamulo.