Kugawana ndi kugulitsana malo a Boma mu Mzinda wa Lilongwe
Khonsolo ya Mzinda wa Lilongwe ikudziwitsa anthu omwe akugawana ndikugulitsana malo mmadera osiyanasiyana mumzindawu kuti kutero ndikuphwanya malamulo a za malo (Land Act 2016) ndiponso a zomangamanga (Physical Planning Act 2016). Khonsoloyi ikuchenjeza iwo omwe akugulitsana ndi kugawana malo ndiponso kumanga mmalowa popanda chilolezo kuti Khonsolo ya Lilongwe idzachotsa katundu womangira (njerwa, mchenga, miyala ndi zina zotero) ndi kuphwanya zomwe anthu angayambe kumanga m’malowa. Khonsolo ya mzindawu, idzatengeranso ku bwalo lamlandu iwo womwe akugawa ndi kugulitsa malo a Bomawa.
Khonsolo ya Mzinda wa Lilongwe ikudziwitsa onse omwe akugula ndi kuyamba kumanga mmalo osiyanasiyana kuti Khonsolo ya Lilongwe siyinapatse wina aliyense mphamvu yogulitsa malo mu mzindawu. Khonsoloyi ikupempha onse omwe akugula malo ndikuyamba kumanga mmadera monga ku Nsungwi (Area 25), m’mbali mwa msewu wa Kaunda (kuchokera pa Gulliver kumapita chaku Area 25), Area 43 ndi madera ena mu mzindawu, kuti asiye kutero pakuti ngati apitiliza, akhala akutaya ndalama zawo mmadzi pakuti zomangamanga zonse zidzachotsedwa (kugumulidwa) ndi Khonsolo ya Lilongwe popanda kupatsidwa chipuputa misonzi chilichonse.
Tiyeni tonse tikonde mzinda wathu ndi ndalama zathu popewa kumanga m’malo a misewu, manda, mitsinje ndiponso omwe sitinapatsidwe motsata ndondomeko zoyenera.