KUBA NDIKUWONONGA KATUNDU WA BOMA
Khonsolo ya mzinda wa Lilongwe ndi yokhudzidwa ndi mchitidwe womwe mzika zina za mzindawu zikuchita pokuba ndikuononga nyali zamu nseu, mawaya a nyali zothandizila magalimoto ndi anthu pa mseu ndi zikwangwani za m’miseu. Izi zikuchitika kwambiri madera awa: area18, 25 ndi 43.
Dziwani kuti zipangizo zimenezi zimathandizila onse oyenda ndi oyendetsa pa mseu komanso zinakhazikitsidwa pofuna kuteteza ndikutsogolera mzika za mzindau.
Khonsoloyi ikudziwitsa onse okhala mu mzinda wa Lilongwe kuti kuononga ndikuba katundu wa boma ndi mulandu. Kotero khonsoloyi ikupempha anthu onse okhala mu mzindawu kuti akhale ndi umwini pa chitukuko china chilichonse komanso aliyense azitha kuyang’anira katunduyi ndikuneneza kwa apolisi kapena kukhonsolo ya Lilongwe onse omwe akukayikilidwa kuti anaba, akusunga ndi kugulitsa katunduyi.
Khonsoloyi igwira ntchito ndi thambi zonse zowona zamalamulo ndikupereka m’manja mwa apolisi wina aliyense yemwe wapezeka akupanga mchitidwe wokuba ndikuwononga katundu wa boma.
Mukafuna kutidziwitsa za mchitidweyu tipezeni motere: tilembereni ku info@lcc.mw kapena kuyimba ku nambala ya ulele ya 346.
Eliam Banda
M’malo mwa Mkulu Woyang’anira Khonsolo ya Mzinda wa Lilongwe