Edit Content

About Us

The Lilongwe City Council was established under the Local Government Act No. 42 of 1998 as a body corporate. The Council comprises the Political and Administrative arms which both derive their authority from the Local Government Act of 1998. The Political  arm is led by the Mayor who is an elected councillor. The mayor is in charge of 27 Wards each overseen by an elected Councillor.  In addition, there are four (4) elected Members of Parliament who represent the Lilongwe urban sector. There are also five (5)  ex-official members representing interest groups. The Administrative arm of Lilongwe City Council is led by the Chief Executive Officer who oversees nine (9) technical departments and devolved sectors, including Commerce & Trade, Engineering, Education, Youth & Sports Sector, Parks & Recreation, Health and Social Welfare Services, Planning & Development and Finance.

Contact Info

KUBA NDIKUWONONGA KATUNDU WA BOMA

KUBA NDIKUWONONGA KATUNDU WA BOMA

Khonsolo ya mzinda wa Lilongwe ndi yokhudzidwa ndi mchitidwe womwe mzika zina za mzindawu zikuchita pokuba ndikuononga nyali zamu nseu, mawaya a nyali zothandizila magalimoto ndi anthu pa mseu ndi zikwangwani za m’miseu. Izi zikuchitika kwambiri madera awa: area18, 25 ndi 43.

Dziwani kuti zipangizo zimenezi zimathandizila onse oyenda ndi oyendetsa pa mseu komanso  zinakhazikitsidwa pofuna kuteteza ndikutsogolera mzika za mzindau.

Khonsoloyi ikudziwitsa onse okhala mu mzinda wa Lilongwe kuti kuononga ndikuba katundu wa boma ndi mulandu. Kotero khonsoloyi ikupempha anthu onse okhala mu mzindawu kuti akhale ndi umwini pa chitukuko china chilichonse komanso aliyense azitha kuyang’anira katunduyi ndikuneneza kwa apolisi kapena kukhonsolo ya Lilongwe onse omwe akukayikilidwa kuti anaba, akusunga ndi kugulitsa katunduyi.

Khonsoloyi igwira ntchito ndi thambi zonse zowona zamalamulo ndikupereka m’manja mwa apolisi wina aliyense yemwe wapezeka akupanga  mchitidwe wokuba ndikuwononga katundu wa boma.

Mukafuna kutidziwitsa za mchitidweyu tipezeni motere: tilembereni ku info@lcc.mw   kapena kuyimba ku nambala ya ulele ya 346.

Eliam Banda

M’malo mwa Mkulu Woyang’anira Khonsolo ya Mzinda wa Lilongwe

Lilongwe City Council

Subscribe Newsletter

Sign up for our latest news & articles. We won’t give you spam mails.

© 2020 Lilongwe City Council. All Rights Reserved