Kuletsa kabaza wa Njinga za moto ndi
zakapalasa mmadera ndi misewu ikuluikulu
mu mzinda wa Lilongwe
Khonsolo ya Mzinda wa Lilongwe ikudziwitsa a kabaza wakapalasa ndi wa njinga zamoto onse kuti ndikoletsedwa kuchita malonda awo mumzindawu mmalo aku Old Town, City Centre ndiponso misewu yonse ikuikulu mumzindawu.
Aliyense yemwe adzapezeke akuyendetsa kabaza wakapalasa kapena wa njinga za moto mmalo ndi misewu yoletsedwayi adzalipilitsidwa chindapusa, ngakhale kumangidwa kumene.
Tiyeni tonse tilemekeze malamulo omwe khonsolo imagwiritsa ntchito pofuna kusamala ndi kuteteza mzika zake kuti tichepetse mpungwepungwe ndi Ngozi zapamsewu.
Mukafuna kudziwa zambiri tipezeni motere: tilembereni ku info@lcc.mw kapena kuyimba ku nambala ya ulele ya 346.
Eliam Banda
M’malo mwa Mkulu Woyang’anira Khonsolo ya Mzinda wa Lilongwe