Kusamuka kwa msika wa nsomba zouma kuchoka ku msika waukulu wa mpanipani kupita ku dela la 25B
khonsolo ya mzinda wa Lilongwe ikudziwitsa onse okhala mu mzindawu zakusamuka kwa msika waukulu wa msomba zouma ku mpanipani kupita ku msika wa 25B. izi zachitika pa zifukwa izi:
- Kufuna kuchepetsa kuthithikana kwa anthu mu msika ngati njira imodzi yopewera kufalikira kwa kachilombo koyambitsa matenda a Covid-19.
- Kufuna kuwonjezera malo osungirapo galimoto zimene zithandizire kuchepetsa kuthithikana kwa njira zodutsa magalimotowa.
- Kufuna kuonjezera nthawi yochitira malondawa kwa anthu ogulitsa nsomba zouma kuti azitha kugulitsa tsiku lonse komanso kuti akhale kufupi ndi malo opikulira nsomba.
Khonsolo ya mzinda wa Lilongwe ikupempha ogulitsa nsomba ndi onse ogula nsomba kuti atsatire ndondomeko imene yakhazikitsidwayi.