YANKHO LA MAVUTO A MAGETSI, KHONSOLO MOGWILIZANA NDI JBR TECHNOLOGY LTD IYAMBA KUPANGA MAGETSI KUCHOKERA KU ZINYALALA
Khonsolo ya Mzinda wa Lilongwe yalowa mugwirizano ndi kampani ya ku India, JBR Technologies Ltd, pa ntchito yopanga magetsi okwana 15 megawatts kuchokera ku zinyalala zomwe zimataidwa Ku Mtaya wake ku area 38.
Ntchitoyi ikuyembekezeka kuthandiza kuchepetsa vuto la zinyalala komanso kuonjezera mphamvu ya magetsi mu mzindawu
Polankhula paulendo woyendera mtayawu, Meya wa mzinda wa Lilongwe, Peter Alex Banda, ayamikira kampani ya JBR Technologies chifukwa cha chidwi chawo chofuna kubwera kampaniyi mu mzinda wa lilongwe. A Banda ati ntchitoyi ibweretsa mwayi wa ntchito kwa anthu ambiri komanso kuthandiza ena kupeza ndalama chifukwa kampaniyo izikhala ikugula zinyalala kuchokera kwa anthu osiyanasiyana.
Ananenanso kuti Khonsoloyi igwirizana ndi maunduna onse okhudzika kuti ntchito yonse yopeleka zilolezo zogwilira ntchitoyi iyende bwino komanso mwachangu. Mmodzi mwa akuluakulu a kampani ya JBR Technologies, Pardeep Singh, ati ndalama zokwana 35 miliyoni US dollars, zilipo kale kukonzekera ntchitoyi. Singh anafotokozaso kuti kampaniyi ili ndi zaka zoposa 40 za ntchito zoteteza chilengedwe kudzera mu makina osamalira zinyalala ndi opanga magetsi.
Khonsoloyi ndi anthu amu mzindawu akuyembekezera kuona ntchitoyi ikuyambika zilolezo zonse zikapelekedwa ndikuyamba kupindula ndi ubale umenewu.