Kwa onse ochita malonda m’malo osavomerezeka ndi khonsolo
Mukukumbutsidwa kuti kuchita malonda m’malo osavomerezeka ndikhonsolo ngati mphepete mwamisewu ndimalo ena otero ndikuphwanya malamulo a Khonsolo.
Motero, Khonsolo ya Lilongwe ikudziwitsa onse ochita malonda m’malo osavomelezedwawa kuti achoke.
Khonsoloyi ikhala ikuchotsa onse omwe akupangira malonda m’malo osavomerezedwawa. Aliyense yemwe adzapezeke akupitiriza kuchita malonda m’malowa adzalipiritsidwa chindapusa ndikulandidwa malonda akewo ngakhale kumangidwa kumene.
Tiyeni tonse tikonde mzinda wathu kuti ukhale wosililika ndi wadongosolo pochitira malonda athu m’malo omwe a khonsolo avomeleza. Komanso tonse ogula malonda tiyeni tipewe kugula zinthu zogulitsidwa m’malo achisawawa.
Mukafuna kudziwa zambiri tipezeni motere: tilembereni ku info@lcc.mw kapena kuyimba ku nambala ya ulele ya 346.
Eliam Banda
M’malo mwa Mkulu Woyang’anira Khonsolo ya Mzinda wa Lilongwe