Ndondomeko zopewera matenda a COVID-19 mu mzinda wa Lilongwe
Malingana ndi gawo (Paragraph) 22 (b) (v) ya Local Government Act Khonsolo imapatsidwa mphamvu yoonesetsa kuti pakhale ndondomeko yakuti matenda asafalikile mu mzinda.
Khonsolo ya mzinda wa Lilongwe ikudziwitsa aliyense okhala mu mzidawu kuti malingana ndi kufala kwa kachilombo koyambitsa ,matenda a Covid-19 ndinso mene chiwerengero cha mliliwu chiliri pakadali pano malingana ndi chikalata chomwe chawulutsidwa ndi Boma la Malawi Lachisanu pa 10 July 2020, tospano khonsoloyi yakhwimitsa ndondomeko zotetezera anthu a munzindawu ku matenda amenewa ndipo igwira ntchito ndi nthambi zachitetezo pofuna kuwonetsetsa kuti aliyense akutsatira ndondomeko zomwe zayamba kugwira ntchito kuyambila lero
Ndondomeko za tsopano zili motere:
1) Kuletsedwa kwa misika imene imapezeka pena paliponse.
2) Kuletsedwa kwa oyenda ndi malonda pali ponse. Motero khosolo ya mzinda wa Lilongwe ikudziwitsa onse omwe akuchita malonda malo osavomelezedwa kuti achoke.
3) Kuimitsidwa kwa malo ogulitsira mowa ndimalo onse azisangalaro. Malo onse ogulitsiramo mowa sadzalolezedwa kuti anthu adzimwerapo mowa kapena kuchezerapo. Malo amenewa adzilolezedwa kugulitsa chakumwa kokha kuyambira nthawi ya 14:00hrs masana mpakana 19:00hrs madzulo
4) Kuimitsidwa kwa maukwati ndi zinkhoswe ndi miyambo ina.
5) Kuimitsidwa kwa mikumano yamasewero ndi ziwonetsero.
6) Kuimitsidwa kwa mikumano ya mapemphero pa malo osadutsa mpweya ndi othithikana .Mikumano yonse ya mapemphero iwonetsetse ndondomeko izi:
a) Kugwilitsa ntchito zotchingira mphuno ndi pakamwa kapena kuti ma mask.
b) Kuwonetsetsa kuti mikumano ya mapempheroyi ikuchitika pamalo odutsa mphepo bwino.
c) Kuthira mankhwala achitetezo pa malo ochitira mikumanoyi komanso zida zonse zomwe zikugwiritsidwa ntchito.
7) Mwambo wamaliro ukuyenera kuchitidwa motsatira malamulo ndi ndondomekoz a Covid -19 makamaka pofuna kudziteteza.
8) Onse oyenda pa galimoto kuphatikizapo ma minibus ndi ma bus akuyenera kutsatira malamulo akakhalidwe malingana ndi bungwe loyanganira za mayendedwe a pa msewu komanso aliyense akuyenera kuvala zozitetezera pakamwa ndi mphuno kapena kuti ma mask. Aliyense akuyenera kutsatira ndondomeko za ukhondo za covid19.
9) Kuimitsidwa kwa mikumano yonse ndipo wina aliyense akuyenera kutenga chilolezo chopangitsira mikumanoyi kwa mkulu woyanganira khonsolo ya mzinda wa Lilongwe.
Khonsolo ya Lilongwe ikupempha wina aliyense ndi amabizinesi osiyana siyana kuti atsatire ndondomekozi mpakana nthawi yomwe tidzalengeze kuti tsopano aliyense sialipachiwopyezo. Khonsoloyi ikutsindikanso kuti nkofunika kuti wina aliyense adziziteteza kukamwa ndi mphuno povala mask.
Yemwe atepezeke akuphwanya malamulowa adzazengedwa mulandu komanso adzamangidwa ndipo onse opanga malonda adzalandidwa ziphatso (Licence) zoyendesera malonda.
Tiyeni tidziteteze, tikhale pakhomo, titsatire ndondomekozi komanso tisakhale pamalo achigulu.
Mukafuna kudziwa zambiri imbani pa nambala iyi 346 mwaulere kapena tumizani uthenga wanu ku info@lcc.mw